Psalms 62

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide.

1Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;
chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.
2Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.

3Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti?
Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba,
ngati mpanda wogwedezeka?
4Iwo akufunitsitsa kumugwetsa
kuti achoke pa malo ake apamwamba.
Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza.
Ndi pakamwa pawo amadalitsa
koma mʼmitima yawo amatemberera.

5Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;
chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
6Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
7Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:
Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
8Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;
khuthulani mitima yanu kwa Iye,
pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.
Sela

9Anthu wamba ndi mpweya chabe;
anthu apamwamba ndi bodza chabe;
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;
iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
10Musadalire kulanda mwachinyengo
kapena katundu wobedwa;
ngakhale chuma chanu chichuluke,
musayike mtima wanu pa icho.

11Mulungu wayankhula kamodzi,
ine ndamvapo zinthu ziwiri;
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
12komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu
molingana ndi ntchito zake.
Copyright information for NyaCCL